First 50 rows of train
| sent_idstring | englishstring | chichewastring | topicstring | sourcestring |
|---|---|---|---|---|
| en1 | Crops need to be planted early as recommended to take advantage of the full rainy season. | Mbewu ziyenera kubzalidwa msanga potsatira malangizo kuti zigwirane ndi nyengo yonse ya mvula | agriculture | agriculture document |
| en2 | With the uncertainty in the rainfall pattern, late planted crops risk moisture stress at critical periods such as increased pest and disease attack, reduced growing period and nutrient uptake | Ndi kusapanganika kwa kagwedwe ka mvula, mbewu zobzalidwa mochedwa zimakhala pa chiopsezo chosowa chinyontho panthawi zofunikira monga kuchuluka kwa matenda ndi tizilombo, kuchepa kwa nthawi yokulira komanso kuyamwa michere munthaka | agriculture | agriculture document |
| en3 | Field preparation should be carried out preferably soon after harvest when the soil is still moist and therefore easy to till | Minda isamalidwe pambuyo pomaliza kukolola pamene dothi lidakali ndi chinyezi ndipo silivuta kulima | agriculture | agriculture document |
| en4 | This ensures deep ploughing and good decomposition of the incorporated crop residues and also improves soil structure and minimizes surface run-off | Izi zimathandiza kuti khasu lidzilowa kwambiri komanso udzu ndi zotsalira za mbewu ziole bwino ndipo nthaka imatakasuka ndi kuchepetsa kuthamanga kwa madzi | agriculture | agriculture document |
| en5 | Where this is not practicable, farmers should aim at having fields ready by the end of September so that they can plant with the first planting rains. | Ngati izi nzovuta kuchita, alimi ayetsetse kukonza minda pofika kumapeto kwa mwezi wa September ndi cholinga chakuti adzabzale ndi mvula yoyamba | agriculture | agriculture document |
| en6 | With the ever increasing cost of chemical fertilizers, proper use of manures becomes more important | Mitengo ya fetelezayakhala ikukwera kotero kagwiritsidwe ntchito koyenera kamanyowa ndi kothandiza | agriculture | agriculture document |
| en7 | Where manures are used in combination with chemical fertilizers, crops grow vigorously. Yields and quality are also improved | Pomwe manyowa akugwiritsodwa ntchito pamodzi ndi feleza, mbewu zimakula mwamphamvu. Zokolola zimachuluka komanso zimakhala zabwino | agriculture | agriculture document |
| en8 | Extension staff should provide technical advice on how to incorporate crop residues, make and use of different types of manure | Alangizi a zaulimi akuyenera kupeleka upangiri wa mmene tingaphatikizire zinyalala za mbewu kuti tipange manyowa a mitundu yosiyanasiyana | agriculture | agriculture document |
| en9 | Weeds deprive crops of plant nutrients, moisture and sunlight. They may also harbor pests and diseases causing reduction in yields. To reduce competition, it is important that farmers weed their crops timely and frequently | Udzu umachepetsa michere, chinyezi ndi dzuwa zofika ku mbeu. Udzu umasunganso tizilombo ndi matenda zomwe zimachepetsa zokolola. Pochepetsa kukanganira , nkofunika alimi apalile mbeu zawo nthawi yoyenera komanso pafupipafupi | agriculture | agriculture document |
| en10 | It is important that farmers use seed and planting material that would germinate, establish well and grow into a healthy crop | Nkofunika kuti alimi agwiritse ntchito mbeu zomwe zingamere, kutakasuka ndi kukula mwathanzi | agriculture | agriculture document |
| en11 | By intercropping, more than one crop can be harvested in the same season from the same plot, thereby obtaining maximum benefit from it | Pobzala mbeu mwakasakaniza, mbeu zopitilira imodzi zikhoza kukololedwa munyengo imodzi pamunda umodzi kotero mlimi amapeza phindu lochuluka | agriculture | agriculture document |
| en12 | In some cases, other benefits include moisture retention, crop support, soil fertility improvement, soil erosion control and pest and disease control | Nthawi zina, phindu lina ndi monga kusunga chinyezi, kupeleka thandizo kumbeu zina, kuwonjezera nthaka/chonde, kuchepetsa kukokoloka kwa nthaka komanso kuthana ndi tizilombo ndi matenda | agriculture | agriculture document |
| en13 | Growing of the same crop on the same piece of land year after year results in poor yields and quality unless expensive management practices are employed | Kubzala mbeu yamtundu umodzi pamalo amodzimodzi kwa nthawi yayitali kumachepetsa zokolola pokhapokha atangieiritsa njira zina zosamalira mbeu zomwenso ndi zofuna ndalama zochuluka | agriculture | agriculture document |
| en14 | For instance continued monocropping in maize fields results in witchweed infestation. It is therefore important that agriculture staff help farmers to work out rotation plans | Mwachitsanzo, kubzala chimanga chokha pamalo amodzi kwa nthawi yayitali kumadzetsa kaufiti. Choncho nkoyenera kuti ogwira ntchito zaulimi athandize alimi ndi ndondomeko zaulimi wakasinthasintha | agriculture | agriculture document |
| en15 | Insect pests and diseases can severely reduce yields and lower the quality of produce | Tizilombo towononga mbeu komanso matenda zimachepetsa zokolola komanso zimatsitsa maonekedwe a zokolola | agriculture | agriculture document |
| en16 | The incidence of pests and diseases can be reduced without necessarily using pesticides but, for example, observing the closed season in tobacco and cotton; burning or burying infested materials away from the field and destruction of volunteer crops | Kupezeka kwa tizilombo komanso matenda kungachepetsedwe posagwiritsa ntchito mankhwala kokha koma mwachitsanzo kutsatira kutha kwa nyengo ta fodya ndi thonje; kuotcha kapena kukwilila zinthu zonse zogwidwa ndi matenda ndi tizilombo komanso kuononga mbeu zina zonse | agriculture | agriculture document |
| en17 | Uprooting tomato, tobacco, or cotton plants after harvesting helps to reduce disease incidence such as nematodes infestation | Kuzula tomato, fodya kapana thonje pakutha pakukolola kumathandiza kuchepetsa kubuka kwa matenda monga mtchemberezandonda | agriculture | agriculture document |
| en18 | A lot of money can be wasted in employing labour and trying to carry out too many tasks at the same time resulting in inefficiency | Ndalama zambiri zikhoza kutayika polemba ogwira ntchito komanso kugwira ntchito zambirimbiri nthawi imodzi zomwe zimadzetsa kusalongosoka | agriculture | agriculture document |
| en19 | Agricultural staff should assist in formulating an appropriate farm plan in agreement with the farmer so that there is efficient use of land, water, labour, time, money and other resources | Ogwira ntchito zaulimi akuyenera kuthandiza pokhadzikitsa ndondomeko za ulimi mogwirizana ndi alimi ndi cholinga chakuti malo, madzi, mphamvu, nthawi, ndalama komanso zinthu zonse zigwire ntchito moyenera | agriculture | agriculture document |
| en20 | With rising costs of farming, it is important to ensure that financial investments bring good returns; optimum crop yields and returns | Ndikukwera kwa zinthu zaulimi, ndikofunika kuonetsetsa kuti ndalama zolowa zikubweretsa phindu labwino; zokolola zapamwamba komanso phindu | agriculture | agriculture document |
| en21 | Research work develop new varieties of crop seed and planting materials to produce varieties which are high-yielding and resistant to pests and disease; to realize the full potential of the improved seed and planting materials, good husbandry practices should be followed | Ntchito ya kafukufuku idzetse mitundu ya mbeu zamakono zosiyanasiyana, zopatsa zokolola zambiri komanso zopilira ku tizilombo ndi matenda; kuti mbeu zamakonozo zichite bwino kwambiri, nkofunika kutsatira ndondomemko zoyenera zamalimidwe | agriculture | agriculture document |
| en22 | Farmers should be aware that high incidences of pests and diseases reduce the yield and quality of crops and should therefore apply various recommended control measures correctly and timely | Alimi azindikire kuti kuchuluka kwa tizilombo ndi matenda kumachepetsa zokolola ndi maonekedwe a mbeu kotero agwiritse ntchito njira zovomerezeka zothana ndi tizilombo ndi matenda moyenera komanso panthawi yoyenera | agriculture | agriculture document |
| en23 | Cultural practices which help to minimize pest problems in the nursery and in the field should be encouraged and farmers should be encouraged to use the Integrated Pest Management (IPM) approach to pest and disease control | Ntchito zachikhalidwe zothandizira kuchepetsa mavuto a tizilombo ku nazale komanso kumunda zilimbikitsidwe ndipo alimi ayenera kugwiritsa ntchito ndondomeko zonse zoyenera zothanirana ndi tizilombo ndi matemba | agriculture | agriculture document |
| en24 | Credit taken to invest in farming is a good idea but farmers need to be assisted by extension staff to calculate gross-margins before getting such credit | Ngongole zotengedwa kuti zitukule ulimi ndi zabwino koma alimi ayenera kuthandizidwa ndi alangizi a zaulimi kuwerengera ndalama zofunika asanatenge ngongoleyo | agriculture | agriculture document |
| en25 | Apart from creating possibilities for rotation, strips can be planted with crops of different pest problems and weather tolerance as a safeguard against crop failure | Kuputula kuthekera kochita kasinthasintha, mizere ibzalidwe ndi mbeu zopilira mosiyana ku tizilombo ndi nyengo kuti titeteze mbeu kusachita bwino | agriculture | agriculture document |
| en26 | The majority of farmers find it very hard to carryout farm operations properly and timely by hand even with hired labour; the use of animal power and animal drawn implements such as tractors, ploughs, ridgers, cultivators and farm carts makes the work easier and faster | Alimi ambiri amavutika kugwira ntchito zakumunda moyenera komanso munthawi yake pogwiritsa ntchito manja ngakhale alembe atchito; kugwiritsa ntchito ziweto komanso zipangizo zokokedwa ndi ziweto monga zogaula, zopanga mizere, zozbalira ndi ngolo zonyamula katundu kumapeputsa ntch… | agriculture | agriculture document |
| en27 | Other farm implements such as sprayers, planters and wheelbarrows also help in farm operations and farmers should aim at acquiring these implements | Zipangizo zina monga zopopera mankhwala, zobzalira mbeu, ndi wilibala zimathandiza pantchito zakumunda ndipo alimi akhale ndi chidwi chopeza zipangizozi | agriculture | agriculture document |
| en28 | Credit taken to invest in farming is a good idea but farmers need to be assisted by extension staff to calculate gross-margins before getting such credit; this would assist in making decision on the amount of credit to get and how to make the most out of it | Ngongole zotengedwa kuti zitukule ulimi ndi zabwino koma alimi ayenera kuthandizidwa ndi alangizi a zaulimi kuwerengera ndalama zofunika asanatenge ngongoleyo; izi zingawathandize kupanga ziganizo choyenera pa kuchuluka kwa ndalama zongongola komanso kagwiritsidwe ntchito kuti a… | agriculture | agriculture document |
| en29 | Crop diversification is the growing of more than one crop by a farmer within the same season or year | Kubzala mbeu zosiyanasiyana kukutanthauza kubzala mbeu zopitilira mtundu umodzi munyengo imodzi kapena chaka chimodzi | agriculture | agriculture document |
| en30 | Where more than one crop is grown in the season, the farmer reduces the risk of total loss of food supply and cash return in the event of some of the crops failing, and also takes care of commodity price fluctuations | Pomwe mbeu zopitilira mtundu umodzi zabzalidwa munyengo imodzi, alimi amachepetsa chiopsezo chosakolola zakudya kapena kusapeza ndalama ngati mbeu zina sidzinachite bwino, ndipo izi zimathandiza kuti mitengo ya zokolola isamasinthesinthe | agriculture | agriculture document |
| en31 | Diversification towards more exportable high value crops such as chillies, tobacco and macadamia also helps farmers realize more cash income, and thus improve their farming while earning foreign exchange into the country | Kuchulukitsa kubzala mbeu zogulitsa kumayiko akunja zamitengo yokwera monga tsabola, fodya, mtedza wamakadamia zimathandizanso alimi kupeza ndalama zochuluka ndipo zimatukula ulimi kwinaku akuthandiza dziko kupeza ndalama za maiko akunja | agriculture | agriculture document |
| en32 | Mixed cropping or intercropping is the growing of more than one crop on the same piece of land | Kubzala mbeu mwakasakaniza kumatanthauza kubzala mbeu zopitilila mtundu umodzi pamalo amodzi | agriculture | agriculture document |
| en33 | Farmers should be encouraged to grow more than one crop in order to harvest more in the same season | Alimi alimbikitsidwe kubzala mbeu zopitilira mtundu umodzi kuti adzikolola zochuluka munyengo imodzi | agriculture | agriculture document |
| en34 | Agroforestry is a collective term for farming system where trees crops and animals are managed on the same piece of land | Ulimi ndi zankhalango ndi ndondomeko zomwe mitengo ndi ziweto zimasungidwa pamalo amodzi | agriculture | agriculture document |
| en35 | The inclusion of tree such as leucaena (Tephrosia vogelli) and msangu (Faidhebia albida) in the farming system is an important part of integrated land use | Kuphatikiza mitengo monga luecaena ndi msangu mu ndondomeko za ulimi ndi njira yofunikira ya kagwiritsidwe ntchito ka nthaka | agriculture | agriculture document |
| en36 | Trees can meet a variety of farmer’s needs as well as contribute directly to the improvement of soil and micro-climatic conditions on the farm | Mitengo imapezetsa alimi zofuna zawo zosiyanasiyana komanso imathandiza kubwezeretsa mphamvu kumthaka ndi zinthu zina zofunika munthaka | agriculture | agriculture document |
| en37 | Both local and exotic breeds are suited and survive in Malawi. The local breeds are suited and survive in Malawi’s environmental conditions but production levels are below those of exotic breeds | Mitundu yachilengedwe ndi yobwera zimalola m'Malawi muno. Mitundu yachilengedwe imagwirizana kwambiri ndi nyengo ya mMalawi muno koma simachita bwino kuposa mitundu yobwera | agriculture | agriculture document |
| en38 | Crossbred animals and poultry perform better than local breeds, but below those of exotic breeds | Mitundu ya ziweto ndi nkhuku zokwatitsa kuchokera kumitundu ina zimachita bwino kuposa zamakolo koma sidziposa mitundu yobwera | agriculture | agriculture document |
| en39 | Smallholder farmers are encouraged to keep local and cross-breeds because exotic breeds require high levels of management | Alimi ang'onoang'ono akulimbikitsidwa kusunga mitundu yamakolo komanso zokwatitsa chifukwa mitundu yobwera imalira kusamala mwapamwamba | agriculture | agriculture document |
| en40 | Different classes of livestock suffer from a number of diseases in various parts of the country, which reduce their productivity | Mitundu yosiyana ya ziweto imadwala matenda osiyanasiyana mmadera a mdziko muno zomwe zimachepetsa kuchulukana kwawo | agriculture | agriculture document |
| en41 | Some diseases affect specific classes while other affects different species of livestock. Some of the livestock diseases can be transmitted to and infect human beings | Matenda ena amagwira mitundu yokhazikika yaziweto pamene ena amagwira mitundu yosiyanasiyana yaziweto. Ena mwa matenda a ziweto amapatsirana ndi anthu | agriculture | agriculture document |
| en42 | Zoonotic diseases include rabies, brucellosis, stomach intestinal worms, tuberculosis and fungal infections. In general, diseased livestock do not eat well, lose body condition and die | Matenda opatsirana pakati pa nyama ndi anthu ndi monga chiwewe, vuto lobereka kunyama, njoka zammimba, chifuwa chachikulu ndi matenda ena. Kwambiri ziweto zogwidwa ndi matenda sidzimadya mokwanira, zimawonda komanso kufa | agriculture | agriculture document |
| en43 | Disease incidences can be minimized through dipping, vaccinations, treatments, good pasture grazing management, meat inspection and restriction in movement of livestock | Kupezeka kwa matenda kungachepe podzisambitsa mankhwala, kudzibaya katemera, kudyetsa moyenera, kuoima nyama komanso kuchepetsa kuyenda kwa ziweto | agriculture | agriculture document |
| en44 | These measures will reduce the risk of contracting specific diseases for both livestock and human beings | Njira izi zichepetsa chiopsezo chopatsirana matenda pakati pa ziweto komanso ndi anthu | agriculture | agriculture document |
| en45 | Farmers are encouraged to improve the quality of their livestock through good management. They are also encouraged to identify markets, which can give them the best returns from their investment in livestock | Alimi akulimbikitsidwa kukuza thanzi la ziweto zawo potsatira ndondomeko zabwino zakasamalidwe. Akulimbikitsidwanso kuti apeze misika imene ingawapezetse phindu lochuluka pa ziweto zawo | agriculture | agriculture document |
| en46 | Where there is potential for irrigation, efforts should be made to utilize irrigable land. In addition to increasing crop yields, irrigation helps reduce the risk of crop failure because of drought and prolonged spells | Pamene pali kuthekera kochita mthilira, alimi ayesetse kugwiritsa ntchito minda yomwe angathe kuthilira. Pamwamba pochulukitsa zokolola, mthilira umathandiza kuchepetsa kusachita bwino kwa mbeu pamene kuli chilala ndi ng'amba | agriculture | agriculture document |
| en47 | Irrigation also assists in livestock production through provision of supplementary water for pasture production as well as drinking water for animals | Mthilira umathandiza pa ulimi wa ziweto popeleka madzi owonjezera paulimi wa chakudya chaziweto komanso madzi akumwa ziweto | agriculture | agriculture document |
| en48 | Proper water management is complementary to good husbandry practices and farmers should be encouraged to manage their water in order to realize increased yields | Kusamala madzi moyenera kumathandizira pa ulimi wabwino ndipo alimi akulimbikitsidwa kugwiritsa ntchito moyenera kuti apeze zokolola zochuluka | agriculture | agriculture document |
| en49 | Sustainable agricultural production in Malawi depends on the rational use of the natural resources in particular soil and water | Ulimi wabwino mMalawi muno umadalira kagwiritsidwe ntchito koyenera ka zinthu zachilengedwe makamaka nthaka ndi madzi | agriculture | agriculture document |
| en50 | Poor soil and water management in agriculture results in poor growth and yield for a number of crop enterprises | Kasamalidwe kosayenera ka nthaka ndi madzi pa ulimi zimazetsa kusakula bwino kwa mbeu ndi kuchepetsa zokolola pa mitundu yosiyanasiyana ya mbeu | agriculture | agriculture document |